Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 280

Paphata pa Chichewa Mwaza ndalama: Kuwononga ndalama. Chitsanzo: Ndinkadziwa kuti akapitirizabe kumwaza ndalama, adzasauka. Mwazirana Makala: Vutana. Chitsanzo: Pamudzi pajatu anthu amwazirana makala. Mwemwetela: Kuonetsa nkhope yachisangalalo. Chitsanzo: Ukumwemwetera chiyani? Mweta: Tenga zonse. Chitsanzo: Pamene ndimafika ndapeza atamwetapo katundu yense. Mwetera pansi: Kuchita mochenjera kwambiri. Chitsanzo: Atambwali ambiri amakonda kumwetera pansi. Mwezi udam’fera: Ali ndi pakati pa mwezi umodzi. Chitsanzo: Mkazi wake mwezi udam’fera. Mwezi wadza ndi thumba: Zodabwitsa. Chitsanzo: Sitikudziwa kuti chichitike n’chiyani, mwezi wadza ndi thumba. Mwinifilimu safa: Mawuwa anayamba potengera zimene zimachitika m’mafilimu kuti munthu yemwe ndi mwinifili- mu samafa nthawi zambiri. Chitsanzo: Zandivuta inde, koma mwinifilimu safa, zidza- yenda. Akita safa: Mawuwa anayamba potengera zimene zim- achitika m’mafilimu kuti munthu yemwe ndi mwinifilimu samafa nthawi zambiri. Chitsanzo: Zandivuta inde, koma akita safa, zidzayenda. Mwinjiro: Mkanjo. Chitsanzo: Anthu a mayiko ena amavala mwinjiro. Myendanazo: Munthu wamiseche, munthu woyenda ndi mabodza. Chitsanzo: (1) Udzasiya kumangouza anthu nkhani ukadzakumana ndi myendanazo. (2) Myendanazo satha phazi pakhomo la ena. 279