Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 28

Paphata pa Chichewa Chera nkhoko: Kuchenjera udakali mwana wamng’ono. Chitsanzo: Ana ambiri masiku ano akumachera nkhoko. Chesula: Mawu amenewa amagwiritsidwa ntchito ponena za zikhulupiriro zomwe anthu a ku Africa kuno amakhala nazo zoti anthu amatha kulodzana. Chitsanzo: N’chifukwa chiyani wayamba kuyenda usiku, akuchesula eti? Cheuka: (a) Yang’ana kumbuyo. Chitsanzo: Akamayenda sacheuka. (b) Kuona chimene chakuthandiza. Chitsanzo: Ukapulumuka m’mavuto umafunika kumacheuka, n’kuona chakuthandiza. Chibaba: Kufunitsitsa kuchita chinachake chomwe unazolowera. Chitsanzo: (1) Ali ndi chibaba cha fodya. (2) Wapeza namwali kuti azidzachengetera chibaba chake. Chibadwire: Osavala. Chitsanzo: (1) Akumazungulira nyumba usiku ali chibadwire. (2) Ngati masitailo sasintha, zaka zikubwerazi anthu azidzangoyenda chibadwire. Chibakera: Khofi. Chitsanzo: Anawamenya chibakera. Chibale chokumba: Chibale chapatali kwambiri. Chitsanzo: Chibale amachikokomezachotu ndi chokumba. Chibalo: Ntchito yopweteka, chilango. Chitsanzo: Amupatsa chibalo choti aime mwendo umodzi mpaka aphunzitsi atuluke m’kalasi. 27