Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 279

Paphata pa Chichewa Mwanditaya: Mwandisiya, simunandilemekeze, mwandinyoza. Chitsanzo: (1) Mwanditaya chifukwa ndilibe ndalama. (2) Mukadzasauka adzakutayani. Mwano: Kukana kuchita zinazake, chipongwe. Chitsanzo: Mwanayu ndi wamwano. Mwanzaneno: Ali wosavala. Chitsanzo: Wamisalayo amangoyenda mwanzaneno. Mwapatalipatali: Kunena mongosankha, kuchita zinthu mongosankha. Chitsanzo: Ndangowauza nkhani ija mwapatalipatali. Mwatchutchutchu: Kuyankhula mosabisa mawu. Chitsanzo: Munthuyu amangoyankhula mwatchutchutchu. Mwatulukamotu m’botolomo! Mawuwa amanenedwa munthu akakhala kuti wadzola mafuta ambiri. Chitsanzo: Koma ndiye mwatulukamotu m’botolomo! Mwaunyinji: Mawuwa amanenedwa ngati anthu ambiri achita zinthu mogwirizana. Chitsanzo: Anthu anabwera mwaunjinji kudzatsanzikana ndi nsangalatsi wawo. Mwauponda: Zakuvutani, mwalephera. Chitsanzo: Ngati mumaganiza kuti mudutsa moyera, mwauponda. Mwaye: Utsi wokakamira kudenga m’khitchini kapena m’nyumba. Chitsanzo: Anthu ena amakhulupirira kuti mwaye ndi mankhwala a m’mimba. Mwayi wanzama: Mwayi waukulu. Chitsanzo: Anzanu apeza mwayi wanzama wofukula ndi manja. Mwaza maso: Kuyang’ana uku ndi uku. Chitsanzo: Ndinamwaza maso koma sindinaone chili- chonse. 278