Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 278

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: (1) Ali ndi mwana wapatchire. (2) Amene ana- berekera limodzi ndi awiri aja, wina uja ndi wapatchire (wapathengo). Mwana wopanda bambo ake: Mwana yemwe wabadwa koma bambo ake sakudziwika. Nthawi zambiri amadziwa ndi maya ake okhawo. Chitsanzo: Ali ndi mwana wopanda bambo. Mwana: Munthu wamkulu koma wosaganiza bwinobwino. Chitsanzo: Bambo ameneyu ndi mwana. Mwanaalirenji: Kusasowa kalikonse, kukhala ndi chili- chonse. Chitsanzo: (1) Pakhomo pakakhala pa mwanaalilenji, ana samanyentchera kapena kutupikana. (2) Pakhomo pawo ndi pa mwana alirenji. Mwanamphepo: Matenda otuluka zilonda zomwe zim- apsa. Chitsanzo: Ameneyu ndi mwanamphepo. Mwandichinya: Mawuwa amenedwa ndi munthu potanthauza kuti munthu wina wamuposa. Chitsanzo: Apatu ndiye mwandichinya, ndalephera kupeza yankho lake. Mwandipinda: Mawu amene munthu amayankhula akakhala kuti sanamvetse zimene wina akunena, kapena ngati wapusitsidwa ndi mnzake. Chitsanzo: (1) Mwandipindatu pamenepa, mukutanthauza chiyani? (2) Ndinakapeza yankho lake, kungoti anandipinda. Mwandisiya m’malere: Simunafotokoze zondikhutiritsa, simunamalize. Chitsanzo: Basi mwamaliza? Apa ndiye mwandisiya m’malere! 277