Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 277

Paphata pa Chichewa anawauza mwakutimwakuti. Mwambo: Zochitika. Nthawi zina mawuwa amagwiritsid- wa ntchito mwachining’a ponena za kudya chakudya. Tanthauzo lake lenileni ndi zinthu zimene mumazichita chifukwa choti munazolowera kapena potsatira zimene zi- nayamba kale kuchitika. Chitsanzo: Mwambotu wayambika m’nyumbamu! Mwamuna mnzako mpachulu: Osamanyoza mwamuna mnzako usakudziwa mphamvu zake chifukwa akhoza ku- kubwanyula. Chitsanzo: Akundiderera? Sakudziwa kuti mwamuna mnzako mpachulu? Mwamvu: Chilimwe. Chitsanzo: Amakonda kupita kutauni m’nyengo ya mwamvu. Mwamwambo: Kungochita chifukwa choti unazolowera kapena ukuyenera kuchita zimenezo basi. Chitsanzo: Ana amene amalephera mayeso amangopita kusukulu mwamwambo basi. Mwana amalira ndi mkodzo wake womwe: Kuchita zin- thu chifukwa chosaganiza bwino kenako n’kumasintha ukudandaula. Chitsanzo: Si paja tinagwirizana kuti ukagwira mtaji usa- masiye, ndiye pano ukubwezanso mawu ako? Ndithudi mwana amalira ndi mkodzo wake womwe. Mwana wachisamba: Mwana woyamba kubadwa. Chitsanzo: Uyu ndi amene anaperekeza, tinakumana naye panjira uja ndiye chisamba. Mwana wamatumbo walira: Njala. Chitsanzo: Mwana wamatumbo walira, tiphike nsima. Mwana wapatchire (wapathengo): Mwana wobadwira ku- chibwenzi kapena amene anabadwa makolo ake asanak- watirane, mwana yemwe wabadwa kunja kwa ukwati. 276