Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 275

Paphata pa Chichewa Muzigona kutali ndi moto: Kuthokoza wina atakuchitira chabwino, mawu amene amanenedwa poyamikira kwambiri, zikomo wamkulu. Chitsanzo: Mwatithandiza zedi, muzigona kutali ndi moto kuti mungapse. Muzikula: Muzichita zinthu ngati munthu wamkulu. Chitsanzo: Muzikula inu, nsinkhu umenewu mung- amasewerebe ndi ana? Mvera m’maso: Kusamvetsetsa zinthu. Chitsanzo: Kodi umamvera m’maso? Monse ndayambira kukuuza muja! Mvera m’mphuno: Kulephera kumvetsa zinthu. Chitsanzo: Kodi mwana wanuyu amamvera m’mphuno? Mvera m’nkhongono: kuchita ulesi. Chitsanzo: Ngati umamvera m’nkhongono, ndi bwino kuti usakwatire. Mvumbi: Kumangoyankhula zambirimbiri osasiya Chitsanzo: Akayamba kuyankhulatu imakhala mvumbi, moti kuti asiye umafunika kungowapatsa bota. Mvundula madzi: Munthu wodanitsa. Chitsanzo: Amvundula madzi amabwera ngati anthu abwino. Mwabwera mwatha: Mwabwera basi palibenso chimene mungachite. Chitsanzo: Mwabwera mwatha, ingolimbani mtima. Mwabwera mwatipeza: Mwabwera basi palibenso chimene mungachite. Chitsanzo: Mwabwera mwatipeza, ingolimbani mtima. Mwachifatse: Modekha. Chitsanzo: Uzichita zinthu mwachifatse. Mwachisawawa: Mopanda dongosolo. Chitsanzo: Sindimafuna kuti anthu amene 274