Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 273
Paphata pa Chichewa
Munatha inu: Zinkakuyenderani kale.
Chitsanzo: Munatha inu, asiyeni anzanu ayendetse zinthu.
Mundifwenthe: Mulote, mudziwe zimene ndikufuna
kuchita.
Chitsanzo: Ngati mukufuna kundidziwa, mundifwenthe.
Mundilinge (mlingo): Mundiyeze, ngati kwa atelala.
Chitsanzo: Atelala mundilinge ndi maso, amunanga
nsanje!
Mungondimaliza: Mungondipha.
Chitsanzo: Mwandilanda munda, ndiye mukufunanso chi-
yani, bwanji osangondimaliza?
Munthu wadiso pamtunda: Wotengeka.
Chitsanzo: Tauni ino sifuna munthu wa diso pamtunda.
Munthu wamba: Munthu wosatchuka, wopanda udindo
uliwonse.
Chitsanzo: (1) Anakana kundithandiza chifukwa ndine
munthu wamba. (2) Salola anthu wamba kulowa malo
amenewo.
Munthu waphula: Wopusa.
Chitsanzo: Munthu amene ndinayenda nayeyo ndi
waphula.
Munthu wazala zazitali: Wakuba.
Chitsanzo: M’tauni mwachuluka anthu a zala zazitali.
Munthu wofaifa: Munthu wopanda mphamvu.
Chitsanzo: Ntchito zotere sizifuna munthu wofaifa.
Munthu wolemberera pamudzi: Wobwera kawirikawiri.
Chitsanzo: Kodi mwana uyu akulembereranji pamudzi
pano?
Munthu wotsika: Munthu wamba, munthu wosauka.
Chitsanzo: Safuna kudzakwatira ndi munthu wotsika.
272