Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 271
Paphata pa Chichewa
Mtimwazire: Munthu woyambitsa mapokoso.
Chitsanzo: Pamudzi pano panali bwino pasanafike
mtimwazire uja.
Mtokoma: Makalata oyenera kutengedwa n’kupititsidwa
kwinakwake.
Chitsanzo: Kwabwera mtokoma wanu.
Mtsala: Zinthu zoti zanenedwa kale.
Chitsanzo: Zimene mukunenazitu ndi mtsala.
Mtsamiro:
(a) Munthu wofa naye.
Chitsanzo: Mukufuna mupite ndi mtsamiro?
(b) Pilo.
Chitsanzo: Tulo timakoma ukayedzeka mutu pamtsamiro.
Mtsikana woyendayenda: Hule, mtsikana wokonda amu-
na.
Chitsanzo: Mtsikanayu ndi woyendayenda.
Mtsinje umalimba ndi miyala: Ukadya mpamene
umapeza mphamvu zoti ukhoza kugwira ntchito.
Chitsanzo: Tiyeni tikadye amwene, mtsinje umalimba ndi
miyala.
Mtsukuluziro: Chimanga chomwe amaika muntchini
akamaliza kugaya mphale kuti atsimikize kuti yonse
yagayidwa.
Chitsanzo: Mukamapita kukagayitsa mphaleyi musaiwale
kutenga mtsukuluziro.
Mtswatswa: Phokoso lomwe limamveka munthu ak-
amaponda masamba ouma, kapena phokoso la mapazi a
munthu akamayenda.
Chitsanzo: Ndinadziwira mtswatswa kuti ndi achimwene.
Mtudzu: Mwano.
Chitsanzo: Sindifuna munthu wamtudzu pakhomo pano.
270