Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 270

Paphata pa Chichewa Mtima wa mtengo: Pakati pa mtengo uliwonse pamakhala polimba kwambiri. Pamenepo pamatchedwa mtima wa mtengo. Chitsanzo: Mtima wa mtengo umakhala wolimba kwambiri moti sungadyedwe ndi chiswe. Mtima wachiwala: Mtima woipa. Mawuwa anabwera ku- chokera ku chiwala. Ukazula mutu wa chiwala, chinachake chakuda komanso chonyansa chimasololoka kuchokera mkati. Amatanthauza munthu amene ama- kusekerera koma akukufunira zoipa mumtima. Chitsanzo: Amakumwetulira pamaso koma ali ndi mtima wa chiwala. Mtima wadwale: Munthu woti sangasinthe, mtima woipa. Chitsanzo: Simungamusinthe amene uja, ali ndi mtima wadwale. Mtima walasa phaso: Kukumbukira kumudzi kapena chinthu china chofunika kwambiri. Chitsanzo: Mpofunika ndibwerere kumudzi, mtima walasa phaso! Mtima wapachala: Munthu wopsa mtima msanga. Chitsanzo: (1) Alitu ndi mtima wapachala. (2) Anthu a mti- ma wapachala amakwatira akazi ofatsa. Mtima wapambali: Munthu wopsa mtima msanga. Chitsanzo: Akutsira mphepotu, ali ndi mtima wapambali. Mtima wasafuliya: Munthu wosachedwa kupsa mtima. Amanena zimenezi chifukwa safuliya sachedwa kutentha. Chitsanzo: Amayi awo ali ndi mtima wasafuliya. Mtima wokhala pakhundu: Kukhala wopsa mtima msan- ga. Chitsanzo: Ali ndi mtima wokhala pakhudu. Mtimam’malo: Usadandaule. Chitsanzo: Mtimam’malo, sangakulande ine ndili pompa- no. 269