Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 27

Paphata pa Chichewa Chaphazi: Ndalama zomwe umapereka kuti munthu akakufunire mankhwala kapena ukamutuma kwinakwake. Chitsanzo: Ngati mukufuna ndipite kukakusakirani mtera, ndipatseni chaphazi. Chatha m’thumba: Wolemera. Chitsanzo: Bambo amene aja ndi chatha m’thumba, akhoza kutithandiza. Chathunthu: Chonse. Chitsanzo: Ndikufuna chimanga chathunthu osati chothyola. Checheta: Kudya momveka phokoso. Chitsanzo: (1) Akuchecheta makaka kuseriko. (2) Chiswe chachecheta matabwa onse. Cheka: Kuthawa. Chitsanzo: Ataona kuti kwavuta anandiuza kuti, “Cheka!” Chengetera: Samalira. Chitsanzo: (1) Muzimuchengetera bwino mwamunayu angakuthaweni. (2) Mkaziyutu amakuchengeterani. Chenjera katalumwa: Kuzindikira pambuyo poti wapusitsidwa kale. Chitsanzo: Akanadziwa sakanamuthandiza. Wachenjera atalumwa. Chenjeza champhongo: Kunyoza kapena kuchitira chipongwe munthu amene amakuthandiza. Chitsanzo: (1) Angandichitire chipongwe chotere? Wachenjeza champhongo, sindidzamuthandizanso. (2) Wachenjeza champhongo, akadzabweranso adzaona kokagona. 26