Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 269

Paphata pa Chichewa (2) Akazi awo amawachitira kamkomya. Nthawi zina amawaphikira mapawo komanso mtenthandevu. Mtera: Mankhwala makamaka azitsamba. Chitsanzo: Asing’anga andipatsa mtera. Mthenga: (a) Ubweya wankhukhu. Chitsanzo: Mphungu sitaya nthenga zake. (b) Munthu wokapereka uthenga. Chitsanzo: Sanabwere, koma atumiza mthenga. Mthirakuwiri: Munthu wabodza yemwe amati akamva nkhani uku, amaitenga n’kukaikhuthura kwina. Chitsanzo: (1) Ndinadzidzimuka nditazindikira kuti amayi amvano aja ndi a nthirakuwiri. (2) Adzakhumudwa akadzazindikira kuti anzawo aja ndi a mthirakuwiri. Mthirakuwiri: Munthu wodanitsa. Chitsanzo: Pamudzi pano pachuluka a mthirakuwiri. Mthyothyo: Kulira kwa kuthyoka kwa timitengo. Chitsanzo: Ndinamvera mthyothyo kuti akubwera. Mtima phaphapha: (a) Kufunitsitsa utamva zinazake. Chitsanzo: Ankangoti mtima phaphapha n’kumandi- yang’ana m’maso. (b) Kuchita mantha. Chitsanzo: Nditamva uthengawo mtima wanga umangoti phaphapha. Mtima suvala nsanza: Mtima umalakalaka zabwino zokhazokha. Chitsanzo: Akuganiza kuti angadzalemere? Zoonadi mtima suvala nsanza! Mtima ukhale m’malo: Kuti ndisiye kuda nkhawa. Chitsanzo: Mpofunika andiuze zotsatira za magazi anga kuti mtima wanga ukhale m’malo. 268