Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 268
Paphata pa Chichewa
Mtcheso: Minga yovuta kwambiri yomwe imakoda ku-
boola chubu cha njinga.
Chitsanzo: Akafuna kukonza njinga zambiri, amapita
pansewu n’kukamwaza mtcheso.
Mtchisi: Munthu wauve.
Chitsanzo: Sindikufuna kuyandikana ndi mtchisi.
Mtemang’ombe: Wodziwa kwambiri kuba komanso
kunama, tambwali.
Chitsanzo: (1) Munthu amene uja ndi mtemang’ombe. (2)
Musakhulupirire mtemang’ombe uja.
Mtembo: Munthu womwalira.
Chitsanzo: Kumotchale kumakhala mitembo yambiri moti
amailongedza m’maalumale.
Mtengatenga: Katundu woyenera kunyamulidwa
n’kupititsidwa kwinakwake.
Chitsanzo: (1) Amagwira ntchito za mtengatenga. (2) Nda-
kumana nawo atanyamula mtengatenga.
Mtengo wazii: Mtengo wotsika, motchipa.
Chitsanzo: Ndagula malaya pamtengo wazii.
Mtengo wozizira: Mtengo wotsika, chotchipa.
Chitsanzo: Nsaluzi ndazigula pa mtengo wozizira.
Mtengo:
(a) Munthu wolimbika pakagwa mavuto.
Chitsanzo: Mapunde ndi mtengo wa pamudzi pano.
(b) Munthu wolemera amene amathandiza anthu ambiri.
Chitsanzo: Munthu amene amathandiza osauka ndi
mtengo wopereka nthunzi.
Mtenthandevu: Tiyi.
Chitsanzo: (1) Munthu wandevu zambiri safunika ku-
mamwa mtendandevu. Anthu amaganiza kuti ndevuzo
zikuyaka kapena amapisirira ndevu zakezo m’kapu.
267