Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 267

Paphata pa Chichewa Msampha: (a) Chinthu chomwe wina amatchera kuti agwire chiachake. Ingakhale nyama kapena munthu. Chitsanzo: (1) Akufuna kukutcherani msampha. (2) Wag- wira mbalame pamsampha. (b) Zimene munthu amanena kapena kuchita kuti alowetse wina m’mavuto. Chitsanzo: (1) Ndinadziwa kuti akunditchera msampha. (2) Ndalama amandipatsa ija inali msampha. Msangwe: Kagulu ka nyenyezi zisanu zowala bwino. Chitsanzo: Kodi unaonapo nyenyezi za msangwe? Msipu uli kukamwa: Kumwalira akubereka. Chitsanzo: Akazi awo amwalira msipu uli kukamwa. Msipu wamera m’khola: Mwayi wopezeka pafupi. Chitsanzo: Koma apa ndiye msipu watimerera m’khola. Msonkhano wa mnzanga alipati: Msonkhano waukulu, wa anthu ambiri. Chitsanzo: Kwa amfumu kunali chimsonkano cha mnzanga ali pati. Msonkhano wa mundipondera mwana: Msonkhano waukulu, msonkhano wa anthu ambiri. Chitsanzo: Atsogoleri a chipanichi amanena kuti kudzaka- la msonkhano wa mundipondera mwana. Msonkhano wandiweyani: Msonkhano waukulu moti sungadziwe onse omwe apezekapo. Chitsanzo: Kuno kuchitika chimsonkhano chandiweyani. Mswachi: Cheyo chotsukira mkamwa. Chitsanzo: Andibera nswachi wanga. Mtanthapalumo: Mawu onena za munthu waukamber- embere. Chitsanzo: Ali kuti mtanthapalumo uja? 266