Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 266
Paphata pa Chichewa
Chitsanzo: Ntchitoyi sifuna mphwephwa.
(b) Mbewu zopanda kanthu mkati monga mtedza kapena
nandolo.
Chitsanzo: Andigulitsa mphwephwa zokhazokha.
Mpira wamtchemberambayi: Mpira wa azimayi kapena
atsikana, mpira wamanja.
Chitsanzo: Mfumukazi yanena kuti ithandiza anthu omwe
amasewera mpira wamtchemberambayi.
Mpishupishu: Kuvutitsa.
Chitsanzo: Akungofuna kundipatsa mpishupishu.
Mpita: Njira yodutsa nyama zakutchire kapena mbewa.
Angatanthauzenso njira yodutsa anthu.
Chitsanzo: Ukamafuna kupha mbewa ndi diwa, umafu-
nika kutchera pampita.
Mpondamakwacha: Munthu wolemera.
Chitsanzo: Achimwene awo ndi mpondamakwacha.
Mpondamatambala: Munthu wolemera. Kale ndalama za-
matambala zidakali zamphamvu, akamatchula munthu
wolemera ankamuti mpondamatambala.
Chitsanzo: Achimwene awo ndi mpondamatambala.
Mpondangolo: Wosabereka.
Chitsanzo: Bamboyu ndi mpondangolo.
Mpotamanja: Chintchito chachikulu, ndewu kapena
nkhondo yaikulu.
Chitsanzo: Ntchito imeneyi ndi mpotamanja.
Mpsimpsi: Kubwezera chipongwe.
Chitsanzo: Mwanayu akuchita mpsimpsi.
Mpungwepungwe: Chisokonezo.
Chitsanzo: (1) Osamapanga mpungwepungwe
angakumangeni. (2) M’tauni muli mpungwepungwe.
Mpwechepweche: Zambirimbiri.
Chitsanzo: Kwathu zakudya ndi mpwechepweche.
265