Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 264

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: Tikakumane pamphambano. Mphangala: Munthu wamphamvu komanso wodziwika, munthu yemwe ambiri amamuopa. Chitsanzo: Amene uja ndi mphangala. Mphasa yopinda nthawi yaitali: Munthu wopanda chikondi. Chitsanzo: M’nyumba mukakhala mphasa yopinda nthawi yaitali, umangokhalira kupirira podikirira tsiku loti udzafe. Mphasa yoyalula tsiku ndi tsiku: Munthu wokoma mti- ma. Chitsanzo: Anthu amenewa akadavutika koopsa, zika- nakhala kuti alibe mphasa yoyalula tsiku ndi tsiku. Mphekesera: Nkhani yosatsimikizika imene anthu ambiri akuikamba mwachinsinsi, nkhani zimene ena amanena zomwe zilibe umboni weniweni. Chitsanzo: (1) Mphekesera zikunena kuti watisiya. (2) Mphekesera zomwe zikumveka ndi zoti bamboyu anakwa- tirapo. Mphemvumdyerakumthiko: (1) Munthu wosauka kwam- biri. Chitsanzo: Safuna kudzakwatiwa ndi mphemvumdyera- kumthiko. (2) Popeza ndine mphemvumdyerakumthiko, ndimangotola zimene atayazo. Mphepo: Matenda a nthomba. Chitsanzo: Ndikuopa kupita kumudzi chifukwa kuli mphepo. Mpherakuleza: Munthu wachinyengo yemwe amanamizira kukuchitira zabwino akufuna kukupusitsa, munthu woonetsa ubwenzi waukulu n’cholinga choti aku- bere.. Chitsanzo: Chikondi akukusonyezanichi ndi chachiphamaso, amene uja ndi mpherakuleza. 263