Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 263

Paphata pa Chichewa Moyo wolowerera: Kukhala ndi khalidwe loipa, kuchita chiwerewere. Chitsanzo: Mwana wawo uja anayamba moyo wolowerera. Moyo wopanikizika: Moyo wovutika. Chitsanzo: Ndikukhala moyo wopanikizika. Moyo wopsinyika (wophinjika): Moyo wovutika. Chitsanzo: Ndikukhala moyo wopsinyika. Moyo wotayirira: Mawuwa amanena munthu amene alibe khalidwe labwino, munthu wakhalidwe lachiwerewere. Chitsanzo: Amakhala moyo wotayirira. Moyo wovuta: Moyo wovutika kwambiri. Chitsanzo: Ku Malawi kuno kuli moyo wovuta. Mpalu: Mlenje. Chitsanzo: Nimurodi anali mpalu woopsa. Mpamba: Ndalama zoyambira bizinezi. Mawuwa angatan- thauzenso zinthu zimene umadalira. Chitsanzo: (1) Moyo ndi mpamba. (2) Ndikhoza kuyamba bizinezi nditapeza mpamba. Mpando wonona: Udindo wabwino, waukulu. Chitsanzo: Analowa m’chipembedzochi chifukwa ankafuna mpando wonona. Mpando wonona: Udindo wobweretsa ndalama zambiri. Chitsanzo: Mipando yonse yonona anapatsa abale awo. Mphambano: (a) Nthawi yoti usankhe chimodzi. Pamphambano ndi ma- lo amene pagawanika njira. Munthu sungadutse njira zonse nthawi imodzi, umafunika kusankha yoti udutse. N’chimodzimodzinso ukakula, umafunika kusankha zin- thu zina pamoyo wako ufune usafune. Chitsanzo: Moyo wanga wafika pamphambano. (b) Malo omwe pakumana kapena kusiya misewu. 262