Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 262

Paphata pa Chichewa (b) Amanenedwanso ngati munthu akunena kuti kulibe zamasewera. Chitsanzo: Lero kuli motomoto. Mowa uli m’mutu: Ataledzera. Chitsanzo: N’chibwana kumayendetsa galimoto mowa uli m’mutu. Moyo kuonera pakhosi: Munthu amene wangotsala pang’ono kufa moti mukudziwa zoti ali moyo poona kuti pakhosi pakutukula. Chitsanzo: Adwala kwambiri moti moyo tikungoonera pakhosipa. Moyo ukupereseka: Kudwala mwakayakaya, moyo ukutha. Chitsanzo: Anabwera kudzationa moyo wa amayi ukupereseka. Moyo wamphale: Moyo wabwino komanso wopanda mavuto. Chitsanzo: “Muli bwanji anzathu?” “Ayi, ife moyo wathu ndi wamphale.” Moyo wamthombozi: Moyo woti pena ziyenda pena sizikuyenda. Nthombozi ndi mtengo womwe umakhala kwina kouma kwina kwakuwisi. Chitsanzo: Ife ndiye bola tikupuma, moyo wathu ndi wamthombozi. Moyo wankhumba: Moyo woyenda kwinaku ukubuula. Chitsanzo: Mmene zinthu zavutiramu, moyo wa anthu ambiri ndi wankhumba. Moyo wawofuwofu: Moyo wofewa. Chitsanzo: Anazolowera moyo wawofuwofu. Moyo wofewa: Moyo wabwino kwambiri. Chitsanzo: Anazolowera moyo wofewa. 261