Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 261
Paphata pa Chichewa
ndikuwayang’anira azichita zinthu mosalongosoka.
Mosapumira: Mosalekeza.
Chitsanzo: Amangwira ntchito mosapumira.
Mosataya nthawi: Mofulumira.
Chitsanzo: Kumachita zinthu mosataya nthawi.
Mosayang’ana nkhope:
(a) Mopanda chisoni.
Chitsanzo: Akhoza kukumenya mosayang’ana nkhope.
(b) Mosakondera.
Chitsanzo: Amathandiza aliyense mosayang’ana nkhope.
Motayirira: Mosadzilemekeza, monyanyira.
Chitsanzo: Azimayi ena amavala motayirira.
Mothinana: Mopanikizana kwambiri.
Chitsanzo: (1) Akaidi amakhala mothinana. (2) M’munda
mwawo muli nthochi zothinana.
Mothithikana: Mopanikizana kwambiri.
Chitsanzo: M’kalasi yathu timakhala mothithikana
Moto wolusa: Moto woopsa kwambiri, wamphamvu.
Chitsanzo: Moto wolusa waotcha nsika.
Moto:
(a) Mawu amene amagwiritsidwa ntchito pouzae ena kuti
anyamuke kapena apitirize. Munthu angathenso kutchula
mawuwa ponena kuti akunyamuka kapena akupitiriza.
Chitsanzo: Bwanayo atakwera galimotoyo, anauza dalaiva
wake kuti, “Moto!”
(b) Munthu wonyankhulayankhula kapena wolongolola.
Chitsanzo: Mkazi amene anakwatira uja ndi moto.
Motomoto:
(a) Mawuwa amanenedwa ngati wina zinthu zikumuyen-
dera kapena ngati akumadya wani m’mudzi kapena pa-
malo.
Chitsanzo: Mnyamata amene uja ndi motomoto.
260