Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 260

Paphata pa Chichewa Mnzanga wa ponda apa mpondepo: Mnzanga wapam- tima, mnzanga amene ndimayenda naye kulikonse. Chitsanzo: Amene uja ndi mnzanga wa ponda apa mpondepo. Mnzanga wabere: Mkazi mnzanga. Chitsanzo: Sindingachite manyazi ndi mnzanga wabere. Mnzati: Munthu wolimba, wothandiza pamavuto, mtengo womwe umachirikiza tsindwi kuti lisalowe mkati. Chitsanzo: (1) Amenewa ndi mnzati pabanjali. (2) Ukachotsa mnzatiwu, dengali liloshoka. Modzitukumula: Monyada, modziyesa wapamwamba, kudzimva. Chitsanzo: Dzulodzuloli amadutsa akuyenda modzituku- mula. Molalo: (a) Kuchemerera. Chitsanzo: Masapota a timu iyi ali ndi molalo. (b) Kukopa mitima ya anthu. Chitsanzo: Munthuyu ali ndi molalo. Monyanyira: Mopitiriza muyezo, mosadzilemekeza. Chitsanzo: (1) Mayiwa amachita zinthu monyanyira. (2) Atsikanawa avala monyanyira. Mopanda dongosolo: Mwachisawawa, mosalongosoka. Chitsanzo: Sindimafuna kuti anthu amene ndikuwayang’anira azichita zinthu mopanda dongosolo. Mosadzilemekeza: Mosadzipatsa ulemu, kuchita zinthu zosayenera, kuchita zinthu ngati mwana. Chitsanzo: Avala mosadzilemekeza. Mosadzimanga: Momasuka. Chitsanzo: Nena mosadzimanga ngati umandikondadi. Mosalongosoka: Mopanda dongosolo. Chitsanzo: Sindimafuna kuti anthu amene 259