Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 259

Paphata pa Chichewa Mlezi: Munthu yemwe amalera mwana wamng’ono mpaka atakula. Nthawi zambiri amakhala wantchito. Chitsanzo: Uyu ndi mlezi wa mwanayu. Mliyenda: Moyenda. Chitsanzo: Akulu anu ali mliyenda. Mlongoti: Mtengo woongoka, pholo. Chitsanzo: Amusenzetsa mlongoti. Mluzu wa galu ndi umodzi: Aliyense amene wamva kuitana asayembekezerenso uthenga wina azingobwera. Chitsanzo: Aliyense akamva kuitana azingobwera, pajatu mluzu wa galu ndi umodzi. Mmangummangu: Mofulumira. Chitsanzo: Tiyeni tizichita zinthu mmangummangu, angatipeze pompano. Mmemo: Nsima yophikidwa pogwira ntchito. Nthawi zam- biri siphikidwa kapena kupakulidwa mwadongosolo. Chitsanzo: Ntchito zolimba ngati izi zimafuna mmemo. Mnefiri: Munthu wamphamvu, wogwetsa, wandewu. Chitsanzo: (1) Mwanayutu akulimbana ndi Anefiri. (2) Amene uja ndi Mnefiri. Mnjunju: Munthu wosamva za ena kapena waliuma. Chitsanzo: Umachedwa kwambiri ukakumana ndi wapolisi wamnjunju pamalo ochitira chipikisheni. Mnkhang’a: Munthu wokakamira. Chitsanzo: Amene uja ndi mnkhang’a, akakumatirira sa- kusiya. Mnyezi: Manyazi. Chitsanzo: Atamugwira akuvuula ndiwo mumphika, anayamba kuchita mnyezi. Mnzanga wa pabondo: Munthu amene umakondana naye kwambiri kuyambira kale. Chitsanzo: Ameneyu ndi mnzanga wa pabondo, tinadziwa- na kale kwambiri. 258