Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 258
Paphata pa Chichewa
(b) Kusafuna kuchoka pamalo.
Chitsanzo: Anthu ambiri amachita mkondwa akapita ku
Jubeki chifukwa choopa kuchita manyazi kuti anthu
awaseka akabwerako chimanjamanja.
Mkuntho:
(a) Kumenya.
Chitsanzo: Njoka simafa ndi mkuntho umodzi.
(b) Mvula ikamagwa mwamphamvu komanso ndi mphepo
timati ikugwa mwankuntho.
Chitsanzo: Dzulo kunagwa chimvula chankuntho.
Mkupamame: Munthu yemwe umapita naye kokafunsira.
Chitsanzo: Ukukumbukira muja ndinabwera kwanu ndi
mkupamame.
Mkute:
(a) Chakudya chomwe chagona, chomwe chinaphikidwa
dzulo.
Chitsanzo: Musandiwerengere phalalo, ine ndidya mkute.
(b) Nkhani kapena ntchito yadzulo.
Chitsanzo: Dzulo tinasungira mkute, tiyeni timalizitse
kaye zimenezo kuti tiyambe za lero.
Mkuzi: Chingwe chomangira buluku kapena siketi kuti
isagwe.
Chitsanzo: Njatani bulukulo ndi mkuzi.
Mleme: Munthu yemwe samaona bwino.
Chitsanzo: Amene uja ndi mleme, maso ake anatha
kalekale.
Mlerakhungwa: Munthu wothandiza kwambiri.
Chitsanzo: Tabwera kwa inu chifukwa tikudziwa kuti
ndinu mlerakhungwa.
Mlesi: Munthu wosakonda kugwira ntchito.
Chitsanzo: Anakwatira mlesi.
257