Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 255
Paphata pa Chichewa
(b) Menya kwambiri.
Chitsanzo: Mwana wojaira amafunika kumuminitsa.
Minyama: Tsoka.
Chitsanzo: Anthu inu ndi amene mukundipatsa minyama.
Miphika siphulana: Amene ali m’mavuto okhaokha san-
gathandizane.
Chitsanzo: Zativuta tonse, miphika siphulana.
Mira pachipande: Nama.
Chitsanzo: Ndinkadziwa ine kuti akumira pachipande.
Misozi ikumuyabwa: Ukufuna kulira.
Chitsanzo: (1) Ngati misonzi ikukuyabwa, bwanji
osaiphinya? (2) Azimayi ambiri misozi ikamawayabwa,
amayamba kuputa amuna awo. Akawamenya amalira mo-
satonthozeka ndipo akamaliza kulirako, amauza amuna
awowo kuti, “Mukufuna ndikakuikireni madzi osamba?”
Misozi ya Farao: Kachaso.
Chitsanzo: (1) Anthu amene amamwa misozi ya Farao
amaderera mitundu ina ya mowa. (2) Atamupeza atauma
ali gwa. Zikuoneka kuti anamwalira atamwa mutu wa
misozi ya farao osadyera.
Misozi yalengeza: Misozi yayamba kuonekera m’maso.
Chitsanzo: Atangomutsina, misozi inalengeza m’maso.
Mitala: Kukwatira mkazi wina uli kale ndi mkazi wina,
kukhala ndi akazi angapo.
Chitsanzo: Bambo wolumala aja anakwatira mitala.
Mithulo: Womana.
Chitsanzo: Mwanayu ndi wamithulo.
Mitsamiro: Wopita naye kumanda.
Chitsanzo: Ena akatenga kachilombo, amakafalitsa kuti
akhale ndi mitsamiro yambiri.
Mituka: Katundu makamaka chakudya chomwe
umatenga paulendo, pokaona athu.
254