Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 254
Paphata pa Chichewa
Chitsanzo: Mwanayu ndi wamiliri.
Mimba ngati dzenje lopanda malire: Wokudya kwambiri.
Chitsanzo: Ali ndi mimba yangati dzenje lopanda malire,
moti inenso ndimadabwa kuti chakudya chonsechi
chimalowa m’thupi mwakemu?
Mimba tiyetiye: Munthu wokonda kudya koma ntchito
ayi. Mawuwa amathanso kugwiritsidwa ntchito ponena
monyoza munthu yemwe akungotsatira anthu koma asa-
kufunidwa.
Chitsanzo: Tawaonerani, ikakwana 12 koloko ndiye mim-
ba tiyetiye, kumabwera kuno kuti adzaipeze itapsa.
Mimba yakhonde: Munthu wa mimba yaikulu.
Chitsanzo: Anthu ambiri olemera amakhala ndi mimba
zakhonde.
Mimba: Kuyembekezera mwana, kukhala ndi pathupi.
Chitsanzo: Mtsikana uja ali ndi mimba.
Mimbulu: Anthu olusa, anthu ovuta.
Chitsanzo: Sindingamakhale ndi mimbulu ili pakhomo pa-
noyi.
Mina: Khaula.
Chitsanzo: Ndachimina, sindidzapitanso kumene kuja.
Minga umabwera ndi mafinya omwe: Pali zovuta palinso
zokoma.
Chitsanzo: Kulima n’kopweteka, komabe osasiya kulima
chifukwa munga umadza ndi mafinya omwe.
Mingoli: Nyimbo, mawu okometsera poyimba.
Chitsanzo: (1) Amakonda kumvetsera mingoli. (2) Mingoli
ya nyimboyi ndi yosangalatsa.
Minitsa:
(a) Lapitsa.
Chitsanzo: (1) Anasiya kuvuta atawaminitsa. (2) Achimina
kuti sadzapitakonso. (3) Anthu akhalidwe lotere
amafunika kuwaminitsa.
253