Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 253
Paphata pa Chichewa
Mgonero: Chakudya chamadzulo.
Chitsanzo: Ndinawapeza akudya mgonero.
Mgugu: Phokoso la mapazi kapena la kugogoda.
Chitsanzo: Kodi mgugu ukumveka kuseriwo ndi wa
chiyani?
Mgula: Mzere wa kumapeto kwa munda kapena m’malire
a malo. Nthawi zambiri umakhala waukulu kwambiri.
Chitsanzo: Tilime mgula apa kuti madzi asaphwasule.
Mgwidyo: Phokoso la madzi kapena zakumwa zina ukam-
ameza.
Chitsanzo: (1) M’kapumutu mwangotsala migwidyo iwiri!
(2) Akamamwa madzi amamveka migwidyo.
Michokocho: Anthu olongolola.
Chitsanzo: Kodi michokocho inali kuseri ija yachoka?
Midenga: Mitsuko.
Chitsanzo: Anyamula midenga akulowera kunsika.
Migolomigolo: Zambirimbiri.
Chitsanzo: Amamwaza ndalama ngati ali nazo migolomigo-
lo.
Mikokoyogona: Akuluakulu apamudzi.
Chitsanzo: Zimene achitazi zaimitsa mitu mikokoyogona.
Mikwingwirima: Mavuto osaneneka, khaulitsa.
Chitsanzo: Akukumana ndi mikwingwirima yambiri. (2)
Atapita kutauni anakumana ndi mikwingwirima.
Milandu siwola: Ukapalamula, mlanduwo umakhalapobe
mpaka utatha.
Chitsanzo: Ankaganiza kuti akathawa tiiwala, mlandutu
suwola!
Miliri:
(a) Matenda omwe amafala mofulumira kwambiri.
Chitsanzo: Masiku ano miliri yangoti mbwee.
(b) Kumana, kuumira.
252