Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 252

Paphata pa Chichewa Meta: Chenjeretsa, kupusitsa. Chitsanzo: Amalonda a masiku ano cholinga chawo chimakhala kumeta anthu kuti apindule. Mezera mate: Osanena kanthu. Chitsanzo: Nkhani zina zimangofunika kumezera mate. Mfana: Mwana. Chitsanzo: (1) Usamachite makani mfana. (2) Mafana am- biri akumachita mano. Mfumu: Mtembo kapena thupi la munthu wakufa. Chitsanzo: (1) Anyakwawa anauza onse kuti aimirire n’cholinga choti atulutse mfumu kuchokera m’nyumba. (2) Amene atapezeke atakhala pansi tikamatulutsa mfumu yathu m’nyumbamu, alipira chindapusa. Mfundo zawedewede: Mfundo zosathandiza, mfundo zosagwira mtima. Chitsanzo: Mfundo zimene amanena ndi zawedewede. Mfundu: Zinthu zimene zimabwera m’mutu khukhu lam’mutu likathetheka. Chitsanzo: M’mutu mwake mumachoka mfundu akamapesa. Mfupidoli: Munthu wamfupi. Chitsanzo: Munthu akakhala mfupidoli, amavutika kutenga zinthu zomwe zili pamwamba. Mfwisuro: Chakudya cha m’mawa. Chitsanzo: (1) Bwerani kuno mufwisure. (2) Tiyeni tikadye mfwisuro. Mgodi: (a) Malo amene munthu amapezako ndalama. Chitsanzo: Umenewu ndi mgodi wanga. (b) Kuchimake. Chitsanzo: Kumeneku ndi kumgodi kwa ndalama. ( c) Phanga Chitsanzo: Anthu onse analowa kumgodi. 251