Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 251
Paphata pa Chichewa
Mederera: Kukonza zinthu bwinobwino, kukongoletsa.
Chitsanzo: Kanyumba kawo kaja akamederera bwinob-
wino.
Memeza: Itanitsa, sonkhanitsa.
Chitsanzo: Ndabwera kudzamemeza anthu kuti apite
kumsonkhano.
Menya m’mimba: Kubera kapena kuchenjeretsa munthu,
kukupusitsa munthu.
Chitsanzo: (1) Anyamata a m’tauni amumenya m’mimba.
(2) Mavenda amumenya m’mimba, amugulitsa foni ya
thonje mkati.
Menya pachifuwa: Kudzitamandira.
Chitsanzo: Anachoka pano akudzimenya pachifuwa.
Menya pansi: Kulephera.
Chitsanzo: (1) Ankayesa kuti ndimupatsa ndalama koma
wamenya pansi. (2) Mukachedwatu mumenya pansi!
Menyerera: Kuyesetsa kuti zinazake zitheke.
Chitsanzo: Ndipita kukamenyerera kuti akutenge.
Menyetsa nkhwangwa pamwala: Kukanitsitsa.
Chitsanzo: Amenyetsa nkhwangwa pamwala kuti sadzapi-
takonso.
Mera mano: Yamba kukalipa kapena kuvuta, kuchoka
chilendo.
Chitsanzo: (1) Simungamudziwe, panotu anamera mano.
(2) Mwayamba kumera mano eti, nanunso mwafika po-
maima pachulu n’kumalalata?
Mera mizu: Kukhazikika.
Chitsanzo: (1) Sikutitu mumere mizu pakhomo pano! (2)
Mkamwini wazintchito ndi amene amamera mizu pakho-
mo.
Meta mpala wopanda madzi: Kuchenjerera kotheratu.
Chitsanzo: Ndikudabwa kuti munthu wanzeru zake ngati
inu mwalola kuti akumeteni mpala wopanda madzi.
250