Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 250
Paphata pa Chichewa
Chitsanzo: Akamayerekedwa azikumbukira kuti chuma
ndi m’chira wa khoswe.
Mdadada: Nyumba zolumikizana.
Chitsanzo: Mdadada wonsewu chimbudzi ndi chimodzi.
Mdala: Mawu onyoza ponena za bambo.
Chitsanzo: Mdalayu ndi khuluku.
Mdidi:
(a) Matenda otuluka thumbo.
Chitsanzo: Akudwala matenda a mdidi.
(b) Kamvekedwe kamapazi poyenda, kugunda.
Chitsanzo: Ndinamva mdidi kuseriku, kodi pali amene
anatuluka panja?
Mdima usaka: Pa nthawi yamasana munthu
umachenjera, koma madzulo umasowa kolowera.
Chitsanzo: Si wathawa, musiyeni, mdima umusaka.
Mdima wa ndiweyani: Mdima waukulu.
Chitsanzo: Magetsi atazima, mnyumbamo munali mdima
wa ndiweyani.
Mdima wa tsokomola ndingakuponde: Mdima waukulu.
Chitsanzo: Mphangalo munali m’dima wa tsokomola
ndingakuponde moti tinkafunika kunyamula miuni.
Mdima: Maliro.
Chitsanzo: Anatithandia kwambiri mdima utatigwera
pakhomo pano.
Mdukamanja: Woduka manja.
Chitsanzo: Kodi mdukamanja uja ali kuti?
Mdyerekezi: Munthu woipa kwambiri. Limenelinso ndi
dzina limene mngelo woipa anavala atagalukira Mulungu
m’munda wa Edeni.
Chitsanzo: Iwe ndiye ndi mdyerekezi ndithu, sumupha
mnzako?
249