Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 25
Paphata pa Chichewa
Chalaka bakha: Chakanika wamkulu mwana
sangachithe, chakanika katswiri ndiye kuti munthu
chisawawa sangachithe.
Chitsanzo: Ngati chalaka bakha ndiye nkhuku ngati iwe
ungatani?
Cham’kuka: Munthu wokonda kukhala pamodzi ndi
akazi.
Chitsanzo: (1) Amene uja ndi cham’kuka. (2)
Athamangitseni a cham’kukawa.
Chamba:
(a) Kupusa, munthu wosokonekera.
Chitsanzo: Inetu sindifuna munthu wachamba.
(b) Mtundu wa nyimbo (gule).
Chitsanzo: Amaimba chamba cha Beni.
(c) Fodya wamkulu.
Chitsanzo: Anavula pansika atasuta chamba.
Chamlomo: Amenewa ndi malipiro amene munthu
amapatsidwa chifukwa choyankhula. Mwachitsanzo
pokafunsira mbeta nthawi zambiri okafunsirawo
amapereka chiwongo kapena chansana kwa makolo a
mkaziyo. Koma kwa munthu amene anayankhula
pokafunsirapo, amamupatsa chamlomo.
Chitsanzo: Tantha mpweya wathu pokulankhulirani
kumene kuja, nafenso tipatseni chamlomo.
Chamseri:
(a) Chakumbali osati pagulu.
Chitsanzo: Akuchita chibwenzi chamseri.
(b) Kuchita zinthu mwachinsinsi.
Chitsanzo: Tiyeni tikumane chamseri.
24