Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 248
Paphata pa Chichewa
(c) Apolisi.
Chitsanzo: (1) Amindibasi akuthawa mbola. (2)
Kutsogoloku kuli mbola.
Mbombo: Munthu womana.
Chitsanzo: Ali kuti mbombo uja? (2) Mwanayu ndi mbom-
bo.
Mbonaona: Mavuto kapena zosautsa.
Chitsanzo: Atamugwira akukhonyola chimanga m’munda
wa eni, anyamata a pamudzipo anamuonetsa mbonaona.
Mbonga: Mpala wotheratu.
Chitsanzo: (1) Anthu ambiri akamachokera kujoni
amabwera atameta mbonga. (2) Ulendo uno ndimetetsa
mbonga.
Mbota: Nsambo, angatanthauzenso zingwe.
Chitsanzo: Ndi katswiri pankhani yokanyanga mbota.
Mbulanda: Ali wosavala, munthu wosavala kalikonse.
Chitsanzo: (1) Mmene anthu akuvalira masiku ano
n’chimodzimodzi kuyenda mbulanda. (2) Chamuchitikira
n’chiyani kuti azingoyenda mbulanda.
Mbuliuli: Chimanga chophulika.
Chitsanzo: Chimanga chimene wakazinga chili mbuliuli zo-
khazokha.
Mbuto: Malo amene munthu amakhala.
Chitsanzo: Mbuto yawo ndi imeneyi.
Mbutuma: Munthu wopusa.
Chitsanzo: (1) Akatsegula pakamwa m’pamene umadziwa
kuti ndi chimbutuma. (2) Anangoona kukula, ndi
mbutuma.
Mbuzi ikakondwa, amalonda ali pafupi: Munthu
ukamavuta ndiye kuti watsala pang’ono kulira.
Chitsanzo: Ndinadziwa ine, kuthamangathamanga kwake
247