Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 247
Paphata pa Chichewa
Mbambande: Chinthu chabwino kwambiri.
Chitsanzo: (1) Malaya amene ndagula ndi mbambande. (2)
Mwana amene uja ndi mbambande.
Mbanda: Chifwamba.
Chitsanzo: Umbanda ukuchuluka m’tauni muno.
Mbava: Munthu wakuba kapena mbala.
Chitsanzo: Mudzasiya chibwana chimenechi
mukadzakumana ndi mbava.
Mbawalagomo: Nyani. Mawu onena mwachining’a omwe
ena amagwiritsa ntchito ponena za nyani. Amagwiritsa
ntchito mawu amenewa akamafuna kumupanga ndiwo.
Nanga aipe ndi dzina lomwe, bola kumupatsa lodyera.
Chitsanzo: Lero aphika mbawalagomo.
Mbewu zacha (zipatso zacha): Zakhwima, zayamba kup-
sa.
Chitsanzo: (1) Chimanga chacha. (2) Mbewu zikayamba
kucha, anthu amanenepa.
Mbiya: Munthu amene sadziwa kusambira.
Chitsanzo: Enafe ndi mbiya, kugwera m’madzi timangopi-
ta pansi ngati mwala.
Mbiyang’ambe: Chidakwa, chiledzerere, munthu
wosachoka pamowa.
Chitsanzo: Ngati ukufuna kuona mbiyang’ambe zenizeni,
pita kwa Mayi Mbiyazapolama.
Mbola:
(a) Mbola ndi kanthu kokhala ngati minga koma
kamatsala pathupi njuchi kapena mavu akakuluma.
Chitsanzo: Njuchi ikaluma imasiya mbola.
(b) Makani.
Chitsanzo: Musiyeni, akakumana ndi anzake amuchotsa
mbola.
246