Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 246

Paphata pa Chichewa mayi akunyumba ngati kuti pali ena akunjira. Chitsanzo: Amenewa ndiye mayi akunyumba. Mazangazime: Mavuto osaneneka, khaulitsa. Chitsanzo: Akabweranso mowa uli m’mutu ndimuonetsa mazangazime. Mazangazime: Zoopsa. Chitsanzo: Anthu olusa amuonetsa mazangazime. Mazenene: Kusamveka bwino, kumveka modukaduka. Chitsanzo: (1) Mawu anu akumveka mazenene lero. (2) Wailesiyi ikumveka mazenene. Mazenene: Kusamveka bwino. Chitsanzo: (1) Wailesiyi ikumveka mazenene. (2) Mawu awo amamveka mazenene. Maziko: (a) Pansi penipeni pa chinthu. Chitsanzo: Maziko a nyumbayi ndi osalimba. (b), pamene nkhani kapena chinthu chachokera. Chitsanzo: Mpofunika tipeze maziko a nkhaniyi. (c), kumanga nyumba. Chitsanzo: Abale anu aja anamanga maziko m’taunimu. Mazoba: Chichewa cha achinyamata chotanthauza amuna kapena anyamata. Chitsanzo: Mazoba enaake amandipatsa moni ngati anamva zoti ndimadya moni ine. Mbadwa: Munthu wobadwira m’dziko kapena dera lina. Chitsanzo: Ife ndi mbadwa za dziko la Malawi. Mbalume: Mfundo zomveka bwino zomwe munthu amanena pofuna kukopa wina. Chitsanzo: Mnyamatayu ali ndi mbalume. Mbalume: Mfundo. Chitsanzo: (1) Akuluwa ali ndi mbalume. (2) Kufunsira ku- mafuna munthu wambalume. 245