Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 245

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: Ndimayesa atsala olongosoka ndi amenewatu, ndiye ayambanso kuba. Ayi ndithu, mavuto si maliro okha! Mavuvu: Kuvuta, kuchita zinthu mwaphuma. Chitsanzo: (1) Mayiyu ndi wa mavuvu. (2) Munthuyu amachita zinthu mwamavuvu. Mawaya anaduka: Saganiza bwino. Chitsanzo: Achimwene anuwa m’mutumu mumakhala ngati mawaya ena anaduka. Mawere awirirana: Kudana kwa pachibale. Chitsanzo: (1) Osamalowerera mawere akawirirana. (2) Ndinapeza pakhomopo pali pokopoko, zikuoneka kuti mawere awirirana. Mwana wapabondo: Mwana wokondedwa. Chitsanzo: Ameneyu ndiye mwana wawo wapabondo. Mawu adakali m’kamwa: Adakayankhula. Chitsanzo: Mawu adakali m’kamwa, anangoona watulu- kira. Mawu apatali: Mawu ozama. Chitsanzo: M’nkhaniyi mwachuluka mawu apatali. Mawu okhadzula: Mawu opweteka komanso amwano. Chitsanzo: Amakonda kuyankhula mawu okhadzula. Uka- wafunsa amanena kuti ndi mmene alili tingowazolowera. Mawu olasa mtima: Mawu opweteka, okhumudwitsa. Chitsanzo: Anandiyankha mawu olasa mtima. Mawu oumitsa pakamwa: Mawu ovuta kuwatchula, mawu otukwana. Chitsanzo: Sindingayerekeze kutchula mawu oumitsa pakamwawo. Mayi akunyumba: Mawu amenewa amanenedwa ndi mwamuna akamauza ena za mkazi wake. Koma azimayi ambiri amadana ndi zoti mwamuna wawo aziwanena kuti 244