Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 244

Paphata pa Chichewa Matudzi (tubzi): Manyi, bibi. Chitsanzo: (1) Ana ena a sukulu amalemba khoma ndi matudzi. (2) Kabudula wakoyu ali ndi matudzi. Matukutuku a pida: Woyankhulayankhula koma alibe mphamvu. Chitsanzo: (1) Atamufwafwantha mpamene ndinadziwa kuti ankangochita matukutuku a pida. (2) Iwe usamachite matukutuku a pida, ndingakuponde! Matukutuku: Kuvuta, kuchita makani. Chitsanzo: Mukamachitsa matukutuku tikuthamangitsani. Matula: Kukubera. Chitsanzo: Mbala zamatula katundu yense wa munthu wolemera uja. Mavu adaning’a onse pakati: Tiyeni tipangane. Chitsanzo: Tiyeni tikumane, pajatu mavu adaning’a onse. Mavunkhomola: (a) Munthu waukali. Chitsanzo: Azichimwene a munthu amene uja ndi mavunkhomola. Udzawapute uone. (b) Mavu akuda omwe amaluma koopsa. Chitsanzo: Amuluma mavunkhomola. Mavuto omiza msinkhu (mavuto oposa msinkhu): Mavuto ochuluka. Chitsanzo: Mavuto amene ndikukumana nawo angotsala pang’ono kumiza msinkhu wanga. Mavuto onenepa: Mavuto aakulu. Chitsanzo: Umakula mopusa ukapanda kukumana ndi mavuto onenepa. Mavuto sakukata: Mavuto sakutha. Chitsanzo: Kungochokera chaka chatha, mavuto sakukata pakhomo pano. Mavuto si maliro okha: Palinso mavuto ena aakulu mofanana ndi maliro. 243