Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 242

Paphata pa Chichewa maso vinitsu. Masomphenya: Kuoneratu zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo. Chitsanzo: (1) Mulungu ankaonetsa anthu masomphenya. (2) Tikufuna mtsogoleri wokhala ndi masomphenya. Masuka ku chipsinjo: Kumasuka ku mavuto, kusiyana ndi munthu wovuta. Chitsanzo: Abwere adzamutenge mwana wawoyu kuti ndi- masuke ku chipsinjochi. Masweswe: (a) Masewera. Chitsanzo: Inetu sindingamachite masweswe ndi iwe, ndine munthu wamkulu. (b) Chiyambi cha dazi. Chitsanzo: Umo mwadutsa masweswemo, ndi umboni wo- ti akhoma malata m’mutumo posachedwapa. Mata phula: Namiza. Chitsanzo: Sindimadziwa kuti akundimata phula. Matako piringidzane: Mawu onena monyoza za munthu wopanda mnzeru yemwe simukufuna mutamuona. Chitsanzo: Awotu akubwera apowo, ali matako piringidzane! Matakoakanapansi: Munthu woyendayenda. Chitsanzo: Amene aja ndi a matakoakanapansi, kamchacha weniweni. Matambala: Ndalama zochepa. Chitsanzo: Phindu limene ndapeza ndi timatambala. Matangadza: Matabwa amene anthu amagwiritsira ntchito pokhaulitsa munthu kuti asamayende kapena kutakataka. Chitsanzo: Ndinawapeza atawamanga m’matangadza. 241