Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 240

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: (1) Ndinakumana nawo ali mapazi potopoto kubwera kuno. (2) Usamangoti mapazi potopoto utipon- dera ufa. Mapepala: Masatifiketi. Chitsanzo: Masiku ano sungapeze ntchito popanda mapepala olongosoka. Mapewa m’mwamba: Kunyada. Chitsanzo: Masiku ano akumayenda mapewa ali m’mwamba. Mapirikaniro: Makutu. Chitsanzo: Mwanayu samva, amakhala ngati walongedza mapirikaniro m’thumba. Mapokoso: Mikangano. Chitsanzo: Sindikufuna mapokoso pakhomo panga pano. Masagwidi: Matenda otupa masaya. Chitsanzo: Akudwala masagwidi. Masanje: Zachibwana. Chitsanzo: Amene mukuchita apawatu ndi masanje. Masautso: Mavuto. Chitsanzo: Akumana ndi masautso ambiri pamoyo wawo. Masiku aja: Kalekale. Chitsanzo: Ndimaona kuti moyo unali bwino masiku aja. Masilamusi: Zamatseka kapena zaufiti. Chitsanzo: (1) Sindimakonda kuonera mafilimu amasilamusi. (2) Anthu amenewa ndi amasilamusi. Maso afiira: Kudikira kopanda kanthu. Chitsanzo: Tiyeni tifulumire tingakapeze maso a makolo atafiira. Maso akuthwa: Amaona bwino kwambiri. Chitsanzo: Ana ake ali ndi maso akuthwa, simungapatsirane chinthu iwo osaona. 239