Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 24

Paphata pa Chichewa Chakudya chili pamphuno: Chakudya chili pafupi. Chitsanzo: Masiku ano chakudya chili pamphuno. Chakudya chogwira pamimba: Chakudya chokhutsitsa. Chitanzo: Mutiphikire chakudya chogwira pamimba. Chakudya chotsakamira m’mano: Chakudya chochepa. Chitsanzo: Chakudya chimene anatipatsa changotsakamira m’mano. Chakufa sichiopa kuola (kutulutsa fungo): Mawuwa amanenedwa munthu akamakumana ndi mavuto ndiye walimba mtima kuti alimbana nawo mosasamala kanthu zomwe akumane nazo. Chitsanzo: Kaya andichotsa ntchito, zawo zimenezo. Chakupha sichiopa kuola (kutulutsa fungo). Chakukhosi: Mawuwa amanenedwa ngati munthu wina ali ndi mawu oti anene koma sanawayankhule. Angatanthauzenso kusunga zifukwa. Chitsanzo: Akazi anu aja ali ndi chakukhosi. Chakumwa cha tsoo (chakumwa cha tswaa): Mowa. Chitsanzo: Kodi mumamwa zakumwa za tsoo? Chakumwa: Mowa. Chitsanzo: Kodi mumachita nacho chakumwa? Chakwanuleka: Ukayenda umayenera kumachita zimene wauzidwa kumene wapita. Malo omwe ukapita umafunika kusiya zimene unazolowera. Chitsanzo: Kumene mwabwera kunotu ndi kwa chakwanuleka. 23