Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 239

Paphata pa Chichewa kutero ndiye kuti mankhwalawo asuluka. Koma ndi zikhulupiriro chabe zimene anthu ambiri akuda amakhala nazo. Chitsanzo: Ndatopa kuzungulira m’zipatala, mundifufuzire mankhwala achikuda. (b) Mankwala ochokera kumitengo. Chitsanzo: Kale kulibe zipatala tinkadalira kwambiri mankhwala achikuda. Mankhwala azitsamba: Mankhwala ochokera ku mitengo, angatanthauzenso mankhwala ochokera kwa asing’anga, mankhwala achikuda. Chitsanzo: Anthu a chipembedzo chimenechi amakana kumwa mankhwala azitsamba. Manong’onong’o: (a) Mphekesela, nkhani imene anthu akukamba mwachinsinsi. Chitsanzo: Pamudzi pano pakumveka manong’onong’o onena kuti mwana uja si wawo. (b) Kuyankhula chapansipansi. Chitsanzo: Ndani akupanga manong’onong’o uko! Manong’onong’o: Mphekesera, nkhani imene ikumveka, nkhani imene anthu akukamba. Chitsanzo: Kodi manong’onong’o akumvekawa ndi a ndani? Manthongo: Zoipa zimene zimasonkhana m’mbali mwa maso munthu ukamadzuka kapena ukamadwala maso. Chitsanzo: Tamuchotsani manthongo mwanayo! Manthu wa mavuto: Mavuto aakulu. Chitsanzo: Chaka chino tikumana ndi manthu wa mavuto. Manyong’olomeza: Tizakudya tokoma. Chitsanzo: Andigulira manyong’olomeza. Mapazi potopoto: Mawuwa amanenedwa ponyoza mmene munthu akuyendera. 238