Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 238
Paphata pa Chichewa
Mangawa: Kugonana muukwati.
Chitsanzo: Akayambana, akazi awo akumawamana man-
gawa.
Mangitsa madzi m’masamba: Kumudikiriritsa munthu
koma osabwera.
Chitsanzo: Tinagwirizana kuti tikumane kumtsinje, koma
nditafikako, ndinazindikira kuti wandimangitsa madzi
m’masamba.
Mangolomera: Mphamvu zambiri, kutemera mankhwala
opangitsa kuti munthu akhale wamphamvu kwambiri.
Nthawi zina amagwiritsidwa ntchito ponena za munthu
amene wapezanso mphamvu.
Chitsanzo: (1) Munthu ameneyu ndi wamangolomera. (2)
Chigoli chimene anamwetsacho chinawapatsa
mangolomera.
Manja a kape (manja a sefa): Manja osasunga kathu.
Chitsanzo: (1) Ali ndi manja a kape. (2) Ali ndi manja a se-
fa.
Manja atherere: Osachedwa kuswa zinthu.
Chitsanzo: Musamupatse matambulawo ali ndi manja ath-
erere.
Manja lende: Ulesi.
Chitsanzo: Mtsikanayu ndi wamanja lende.
Manja: Munthu yemwe amati akabzala mbewu
zimabereka bwino.
Chitsanzo: (1) Onani maungu kukula ngati mutu wa
munthu. Azakhalitu muli ndi manja abwino. (2) Agogo
mudzale ndinu, muli ndi manja a maungu.
Mankhwala achikuda:
(a) Makhwala azitsamba, mankhwala omwe nthawi
zambiri amakhala ndi zizimba zake. Amatha kukuuza kuti
ukamwere m’chipande, ukamwere pakhomo kapena
ukamwe utavula malaya. Amakhulupirira kuti akapanda
237