Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 237

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: (1) Sindidzamugulanso, amakonda kuchita malonda a mphaka. (2) Mukuti ndigule katunduyo ndisanamuone. Amenewatu ndi malonda a mphaka. Malovu m’kamwa nde: Kusowa chonena. Chitsanzo: Atamufunsa anangoti malovu m’kamwa nde! Maluli: Kusaphonya. Chitsanzo: Pamudzi pano pali anyamata amaluli, saponya mwala pachabe. Maluwa a dziko: Akazi Chitsanzo: Mukamangoti maso m’mwamba mupita, akazitu ndi maluwa a dziko! Simungawakwanitse onse. Mambala: Tambwali, wakuba. Chitsanzo: Munthu ameneyu ndi mambala. Mamulumuzana: Anthu wachikulire, olemekezeka. Chitsanzo: Kumsonkhanowo kunabwera mamulumuzana. Mana: Zinthu zaulere. Mawuwa anachokera ku Mana yemwe ankagwa m’chipululu pamene Aisiraeli ankapita ku Kanani. Chitsanzo: Chaka chino mana watigwera. Mandevu: Munthu wandevu zambiri. Chitsanzo: Mwawaona a mandevu aja? Manga lamba: Kulimba nazo, kulimbikira. Chitsanzo: Amene akufuna kupambana ayenera kumanga lamba. Manga m’phukusi: Kukubisira. Chitsanzo: Zimene anafotokoza sizimamveka bwinobwino, wangotimanga m’phukusi. Manga mlaza m’maso: Kulimba mtima, kusachita manyazi. Chitsanzo: Nditaona kuti anthu akundiseka, ndinangomanga mlaza m’maso. 236