Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 236

Paphata pa Chichewa Malipsata: Ali maliseche, osavala. Chitsanzo: (1) Anamuyendetsa mudzi wonse ali malipsata. (2) Akumazungulira nyumba usiku ali malipsata. Malirom’mbale: Ndiwo ya nyama. Chitsanzo: (1) Ife ndiye malirom’mbale timawalawira m’maukwati kapena m’masadakamu. (2) Ndiwo zake zikakhala malirom’mbale, amabisa mphika kuchipinda. Maliseche: (a) Malo obisika. Chitsanzo: Ndi bwino kumalangiza ana anu kuti anthu ena asamawagwire maliseche. (b) Wosavala. Chitsanzo: Anthu ambiri akapita kunyanja amangoyenda maliseche. Malo athyathyathya: Malo afulati, Malo opanda chi- tunda. Chitsanzo: Ndikufuna kugula malo athyathyathya, osati paphiri. Malo athyathyathya: Malo opanda chitunda, malo afulati, chigwa. Chitsanzo: (1) Masewera amenewa amakhala bwino pamalo athyathyathya. (2) Ulimi umakoma pamalo athyathyathya. Malo obisika: Kumaliseche. Chitsanzo: Osamavala zovala zoonetsa malo obisika. Malo osayenera: Maliseche, malo obisika. Chitsanzo: Usadzalowe kuti munthu wina akugwire malo osayenera. Malodza: Zodabwitsa, zachilendo. Chitsanzo: Chaka chino tiona malodza ndithu, ndi awa omwe kugula njinga? Malonda a mphaka (chona): Malonda okayikitsa, malon- da achinyengo, kugulitsana kanthu komwe sunakaone. 235