Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 234
Paphata pa Chichewa
(b) Kukula mtima.
Chitsanzo: Mwana uyu ndi wamakani ngati mfiti.
Makanja: Munthu wamtali. Dzinali linachokera ku gule
wamtali kwambiri wotchedwa makanja.
Chitsanzo: Ana omwe anabereka ndi makanja.
Makata: Zinthu zophikidwa zili zaziwisi monga nandolo,
nzama kapena mtedza.
Chitsanzo: Lero tidya makata a nandolo.
Makedzana: Kalekale.
Chitsanzo: Amakonda nyimbo zamakedzana.
Mphunomphuno: Zambirimbiri.
Chitsanzo: Chakudya pakhomo pawo ndi mphunophuno.
Makhulululira: Kubwera onse ndi ana omwe.
Chitsanzo: Pobwera kumeneko mukangochita
makhululira.
Makobiri:
(a) Ndalama.
Chitsanzo: Chimene ndinabwerera m’tauni muno ndi
kudzapanga makobiri.
(b) Ndalama zasiliva.
Chitsanzo: Anamugulitsa mnzake ndi makobiri 30 asiliva.
Makono: Masiku ano.
Chitsanzo: Makono, anthu asiya chikhalidwe chawo.
Makonzedwe:
(a) Zimene mwakonza kuti muchite.
Chitsanzo: Papangidwa makonzedwe oti mupite
kunyumba.
(b) Kuphika chakudya makamaka nsima.
Chitsanzo: Musanyamuke, mayi akupanga makonzedwe
kuseliku.
Makosana: Azibambo.
Chitsanzo: Ndinakumana ndi makosana awiri akugulitsa
makhamisolo.
233