Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 233
Paphata pa Chichewa
Maganizo obwerera m’mbuyo: Mfundo zosathandiza.
Chitsanzo: Angokula koma amaganiza mobwerera
m’mbuyo.
Maganyu: Ntchito zosadalirika.
Chitsanzo: Masiku ano ndimangogwira maganyu.
Magawano: Kusagwirizana.
Chitsanzo: M’banjamu muli magawano.
Magule andiweyani (ankhaninkhani): Magule ambirimbi-
ri.
Chitsanzo: (1) Pamwambowo panavinidwa magule ankha-
ninkhani. (2) Kukhala mpikisano wa magule andiweyani.
Magwero: Chiyambi, pochokera.
Chitsanzo: Nkhaniyi magwero ake ndi amenewa.
Magweru:
(a) Munthu yemwe mano ake ena anaguluka.
Chitsanzo: Anthu ambiri ochita masewera a nkhonya
amakhala amagweru.
(b) Malo opanda kanthu.
Chitsanzo: Chimanga cha magweru chimavuta kutong’ola.
Maimvaimva: Kumangomva zonena za ena.
Chitsanzo: Musamale ndi maimvaimva, anthu
akusokonezerani banja.
Makamaka: Kutsimikizira mfundo inayake.
Chitsanzo: Umapindula ndi maphunziro makamaka ngati
umafunadi kuphunzira.
Makamu: Ambirimbiri, zambirimbiri.
Chitsanzo: Kumwamba kuli makamu a angelo.
Makanda: Ana aang’ono.
Chitsanzo: Akundiputa ndi makanda omwe.
Makani:
(a) Mpikisano.
Chitsanzo: Ndani atapambane pa makani olikhana
komanso kugwetsanawa?
232