Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 232

Paphata pa Chichewa Madoda: Anthu akuluakulu, anthu audindo. Chitsanzo: Kodi madoda ali panjawa abwera kudzatani? Madyeramphoto: Anthu okonda kupereka kapena kulandira ziphuphu, anthu omwe amafuna kudya zaulere, anthu omwe amachita zautambwali. Chitsanzo: Anthu a khalidwe la umadyeramphoto akuchuluka masiku ano. Madyerero: Phwando. Chitsanzo: Kwathu kuli madyerero. Madzalamphuno: Munthu woyankhula zosamveka. Chitsanzo: Zoona mungabwere ndi madzalamphunoyu. Madzi achita katondo: Pavuta, zasokonekera. Chitsanzo: Nditaona kuti madzi achita katondo, ndinangochokapo. Madzi afika m’khosi: Zinthu zavuta. Chitsanzo: (1) Ndikuona kuti zitivuta tikayamba ku- chitapo kathu madzi atafika m’khosi. (2) Tiyeni tisamuke madzi asanafike m’khosi. Madzi akali m’nkhongono: Zisanavute. Chitsanzo: (1) Ndi bwino tidziwiretu chochita madzi akali m’nkhongono. (2) Tiyeni tithane ndi vutoli madzi akali m’nkhongono. Madzi m’kulubza mchenga upita pamwamba: Kunena zinthu mwachinsinsi. Chitsanzo: Sitimadziwa kuti madzi m’kulubza mchenga upita pansi. Onsewa akudziwa ndithu. Mafana: Ana, anthu osadziwa zambiri. Chitsanzo: Kodi mafana aja ali kuti? Mafilimu: Munthu yemwe amachita zautamwali ama- munena kuti ndi wamafilimu. Chitsanzo: Mwanayu ndi wamafilimu. 231