Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 231
Paphata pa Chichewa
M’mimba ndi n’chipala: Chipala ndi malo omwe anthu
amasulirapo zinthu zosiyanasiyana monga makasu,
nkhwangwa, mipeni ndi zina. Chifukwa choti pachipala
pakhoza kupangidwa chilichonse, amayerekezera m’mim-
ba kuti munthu akhoza kubereka mwana wovuta ndi
wabwino ndi mimba imodzi yomweyo.
Chitsanzo: Ukakaona kusiyana kwa khalidwe lawo
ukamvetsadi kuti m’mimba ndi m’chipala.
M’mwamba: Mumtengo.
Chitsanzo: Osamakwera m’mwamba.
M’thengo mudalaka njoka: Kwanu ndi kwanu, ngakhale
patatenga nthawi yaitali bwanji umadzabwererako.
Chitsanzo: Asiyeni abwerako, m’thengo mudalaka njoka.
M’tupatupamu: Mawu amene amanenedwa ngati munthu
sakufuna kunena kumene wapeza zinazake. Mawuwa ndi
ofanana ndikunena kuti “kwinakwake.”
Chitsanzo: “Mwazitenga kuti ndalamazi?”
“M’tupatupamu.”
Mabebi: Mawu omwe achinyamata amanena akamanena
za akazi.
Chitsanzo: Mabebi ambiri ndi a milomo yokhala ngati
achita kusongola.
Mabonzo: Mafupa.
Chitsanzo: Ndinapeza atamaliza ndiwo zonse, moti
ndinangopeza mabonzo okhaokha.
Machawi: Changu.
Chitsanzo: Chitani machawi tingachedwe.
Madala: Bambo wachikulire.
Chitsanzo: Madala andituma kuti ndikawagulire mowa.
Madobadoba: Anthu omwe amangoyendayenda m’tauni
osadziwika bwino zochita zawo.
Chitsanzo: M’tauni muno muli madobadoba omwe
cholinga chawo n’kupusitsa anthu.
230