Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 23

Paphata pa Chichewa Chabwalo: Ndalama zomwe anthu amalipira kuti mlandu wawo uweruzidwe. Chitsanzo: Kuti tiweruze mlanduwu, perekani kaye chabwalo. Chadza ndi yani? Mawu omwe anthu amanena podabwa chifukwa chake wina wachita zinazake zachilendo. Chitsanzo: Chadza ndi yani kuti mulowe m’nyumbamu ndi masilipasi? Chafutambuyo: Mobwerera kumbuyo. Chitsanzo: Akuyenda chafutambuyo. Chagona apa: Pamene pali nkhani. Chitsanzo: Chinsinsi chake chagona apa. Chagona pati: Pamene pali nkhani. Chitsanzo: (1) Kodi chinsinsi chake chagona pati? (2) vuto lagona pati? Chakachadza: Munthu amene amati akabereka mwana, mwanayo amamwalira. Chitsanzo: Akazi anuwa ndi a chakachadza. Chakachika: Kusowa ndalama, kusauka kwambiri. Chitsanzo: (1) Atsikana akuno akufuna anyamata okongola m’nthumba, osati ochakachika. (2) Amukana chifukwa ndi wochakachika. Chakhola: Chiweto chimene munthu amapereka kwa eni khola pothokoza kuti awawetera ziweto zawo m’khola lawo. Chitsanzo: Musanatenge mbuzi zanu, perekani kaye chakhola. 22