Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 229

Paphata pa Chichewa Lungama: Kukhala munthu wopanda cholakwa, kusalakwitsa kanthu. Chitsanzo: Padziko lapansi palibe munthu wolungama. Lunjika: Yenda moloza chinachake, loza chinthu, yang’ana chinthu, ponya moloza chinachake. Chitsanzo: amayenda molunjika ineyo. Luntha: Khama. Chitsanzo: Sukulu imafuna munthu waluntha. Lusifala: Munthu woipa kwambiri. Chitsanzo: Sindimadziwa kuti bambowa ndi Lusifala Lusifala: Munthu woipa, Satana. Chitsanzo: (1) Munthu amene uja ndi lusifala. (2) Lusifala anathamangitsidwa kumwamba. Luzi m’nkhosi: Kukalamba, makwinya a ukalamba. Chitsanzo: Amayi okongola aja anangotsala ndi luzi m’nk- hosi. 228