Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 228
Paphata pa Chichewa
Luma chiputu (gwira chiputu): Kanirira.
Chitsanzo: (1) Ndinamuuza kuti atuluke m’nyumbamo
koma akuluma chiputu. (2) Mkamwini uja anagwira
chiputu, safuna kuchoka pamudzi paja.
Luma khutu (tsina khutu): Kuulula pang’ono.
Chitsanzo: (1) Kodi anakutsinani khutu zokhudza ulendo
uja? (2) Andiluma khutu za nkhaniyi ndi achemwali anga
aja.
Luma mano:
(a) Kufa utadwala.
Chitsanzo: Sizimakhala zodandaulitsa kwambiri nkhalam-
ba ikaluma mano.
(b) Kuchita khama (kunyindirira).
Chitsanzo: Pogwira ntchito umafunika kuluma mano.
Lumana chala: Kupangana kuchita chinthu chimodzi.
Chitsanzo: Ngati tikufuna zitiyendere, tifunika tilumane
chala.
Lumana: Kudana.
Chitsanzo: (1) Akagwirizana alekeni, mawa
adzalumananso. (2) Mabwenzi apamtima aja analumana.
Lumira mlomo: Limbikira.
Chitsanzo: Ntchitoyi ndi yovuta moti ndi yofunika
kulumira mlomo.
Lumo: Mpeni, chinthu chakuthwa.
Chitsanzo: Lamucheka ndi lumo.
Lumphitsa mpanda: Kuchititsa kuti athawe.
Chitsanzo: Akuba anabwera aja awalumphitsa mpanda.
Lungalunga: Munthu wabwinobwino wopanda chilema.
Chitsanzo: Ukakhala walungalunga osamatha mawu,
chilemba chimachita kubwera.
Lungalunga: Munthu wopanda chilema.
Chitsanzo: Lungalunga n’kubadwa, chilema chidza kuusa-
na.
227