Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 227
Paphata pa Chichewa
Lowa m’vwivwi: Kulowa m’gulu.
Chitsanzo: Wakubayo ataona kuti anthu ayamba
kumuthamangitsa, anangolowa m’vwivwi ndipo
sanaonekenso.
Lowa: Kumuyesa mnzako kapena munthu wina,
kusalemekeza munthu, kunyoza munthu.
Chitsanzo: Sindimafuna kuti munthu azindilowa.
Lowe: Malo odikha madzi, malo otsika.
Chitsanzo: Mpunga umachita bwino palowe.
Lowerera:
(a) Kusokonekera, kukhala ndi khalidwe loipa, kusamva.
Chitsanzo: Mwanayu ndi wolowerera.
(b) Kusowa, kuzemba, kulowa m’chigulu.
Chitsanzo: Wangolowerera m’chigulu.
Lowetsa mutu m’phiko: Kukhala ngati sukuona.
Chitsanzo: Pamene ndimafuna ndimukodele
anangolowetsa mutu m’phiko.
Loza chala (veka mlandu): Kuimba munthu wina mlan-
du.
Chitsanzo: Mukayambana m’banja, zimakhala bwino kuti
mungokambirana m’malo momalozana chala (momaveka
wina mlandu).
Loza ndege ndi chala: Nyada.
Chitsanzo: (1) Akazi awo aja anasintha kwambiri moti
masiku ano amaloza ndege ndi chala. (2) Kodi tikalemera
ndiye tiziloza ndege ndi chala?
Loza nthiko: Kumbukira kumudzi.
Chitsanzo: Atakhala kwa miyezi ingapo, bamboyo analoza
mthiko.
Luma chala: Khala duu osanena kanthu, kusaulura
nkhani.
Chitsanzo: (1) Atamva nkhaniyo ndinangoluma chala. (2)
Ukawamva akukamba nkhani imeneyi, ungoluma chala.
226