Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 225

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: Ataona kuti zavuta, analiyatsa liwiro la mtondowadooka. Liwiro: Wachimasomaso, wadama, wokonda amuna kapena akazi. Chitsanzo: Mkazi akakhala wa liwiro, amuna samufunsira. Liwongo: Mlandu. Chitsanzo: Sindikufuna kuchita nawo zimenezi, ndikuopa kukhala ndi liwongo la magazi. Lizita: Khama loopsa. Chitsanzo: (1) Munthu uyu ndi wa lizita. (2) Kukhala ndi lizita n’kukhalanso mbuli ndi nsakanizo woopsa. Lodza: Mawu amenewa amagwiritsidwa ntchito ponena za zikhulupiriro zomwe anthu a ku Africa kuno amakhala nazo zoti anthu amatha kuchititsa kuti mnzawo afe kapena akumane ndi tsoka linalake. Angatanthauze ku- chita mankhwala kuti wina adwale. Chitsanzo: Ukufuna uyambane ndi ine eti, ndikuphwan- yatu! Akulodza eti? Lola opanda mano: Mwayi kugwera anthu opanda omwe sakuufuna. Chitsanzo: Taonani katundu apezayu? Koma zoonadi chimanga chimalola opanda mano. Lololo: Zambirimbiri. Chitsanzo: Ndalama ndili nazo lololo. Longa diso momwe: Thandiza kwambiri. Chitsanzo: Mwana ameneyu ukamusamalira bwino adzakulonga diso momwe. Lowa chamwaka: Kudwaladwala. Chitsanzo: Amalume sakupeza bwino, alowa chamwaka. Lowa libolonje (njobwe): (a) Kudwaladwala. 224