Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 224
Paphata pa Chichewa
(b) Kupirira.
Chitsanzo: Limbani mtima mayi, zamoyo ndiye palibe apa.
Limba nazo: Kuchita khama, kupirira.
Chitsanzo: (1) Mavutowa akufunika kulimba nazo. (2) Ban-
ja ndi limeneli koma mpofunika mulimbe nazo.
Linda zidzale (dikira kuti zidzaze): Kuzengereza.
Chitsanzo: Matendawa anachedwa nawo chifukwa
amalinda zidzale (amadikira kuti zidzadze).
Linunda: Chilema cha pamsana.
Chitsanzo: Ndimayesa aberekera chikwama osadziwa kuti
ndi linunda.
Lipira fundudwa: Lipira tchimo lamwini.
Chitsanzo: Muzichenjera ndi atsikanawa, mungadzalipire
fundudwa.
Lira ching’ang’adza (lira mayi wawaye): Lira mosa-
tonthozeka.
Chitsanzo: Analira ching’ang’adza chitedze chitamu-
yabwa.
Lira msampha utaning’a: Kutopa utatsala pang’ono
kumaliza kapena kutuluka m’mavuto.
Chitsanzo: Nguluwe inalira msampha utaning’a.
Litcholotcholo: Chofiira chapamutu pa tambala.
Chitsanzo: Chili pamutu pa tambalayo si moto, koma
litcholotcholo.
Litchowa: Chinthu chimene ena amagwira m’manja,
nthawi zambiri chimakhala mchira wa nyama kapena
chimapangidwa ndi ubweya wa nyama.
Chitsanzo: A Kamuzu Banda ankanyamula litchowa.
Liuma: Kusatsutsika, kusangonja, kumva zako zokha.
Chitsanzo: Sindingalole kumakhala ndi munthu waliuma.
Liwiro lamtondowadooka: Kuthamanga kosacheuka
m’mbuyo, liwiro loopsa.
223